Oweruza 8:22-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Pamenepo anthu a Israyeli anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m'dzanja la Amidyani.

23. Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.

24. Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse ali yense mapelele mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao mapelele agolidi, pokhala anali Aismayeli.

25. Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo cobvala, naponyamo yense mapelele a mwa zofunkha zao.

26. Ndipo kulemera kwace kwa mapelele agolidi adawapempha ndiko masekeli cikwi cimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zobvala zacibakuwa za pa mafumu a ku Midyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamila zao.

27. Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mudzi mwace, ndiwo Ofira; ndi Israyeli yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yace ngati msampha.

28. Motero anagonjetsa Amidyani pamaso pa ana a Israyeli, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni.

29. Ndipo Yerubaala, mwana wa Yoasi anamuka, nakhala, m'nyumba ya iye yekha.

30. Nakhala nao ana amuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.

31. Ndipo mkazi wace wamng'ono wokhala m'Sekemu, iyenso anambalira mwana wamwamuna; namucha dzina lace Abimeleki.

Oweruza 8