20. Nati kwa Yeteri mwana wace woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolola lupanga lace; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.
21. Pamenepo Zeba ndi Tsalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yace. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Tsalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamila zao.
22. Pamenepo anthu a Israyeli anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m'dzanja la Amidyani.
23. Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.
24. Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse ali yense mapelele mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao mapelele agolidi, pokhala anali Aismayeli.