1. Ndipo amuna a Efraimu anati kwa iye, Ici waticitira nciani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidyani? natsutsana naye kolimba.
2. Koma ananena nao, Ndacitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efraimu sikuposa kuchera mphesa kwa Abiezeri?
3. Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midyani, Orebi ndi Zeebi, ndipo ndinakhoza kucitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.
4. Ndipo Gideoni anafika ku Yordano, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali cilondolere.
5. Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndirikulondola Zeba ndi Tsalimuna mafumu a Midyani.
6. Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?