Oweruza 4:23-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Momwemo Mulungu anagonjetsa tsiku lija Yabini mfumu ya Kanani pamaso pa ana a Israyeli.

24. Ndipo dzanja la ana a Israyeli linamkabe ndi kulimbika pa Yabini mfumu ya Kanani mpaka adamuononga Yabini mfumu ya Kanani.

Oweruza 4