Oweruza 3:19-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndiri nao mau acinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani cete. Ndipo anaturuka onse akuimapo.

20. Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'cipinda cosanja copitidwa mphepo, Nati Ehudi, Ndiri nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wace.

21. Ndipo Ehudi anaturutsa dzanja lace lamanzere nagwira lupanga ku ncafu ya kulamanja nampyoza m'mimba mwace;

Oweruza 3