Oweruza 20:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Pamenepo ana a Benjamini anaturuka m'Gibeya, naononga a Israyeli tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi,

22. Koma anthu, ndiwo amuna a Israyeli, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.

23. Ndipo ana a Israyeli anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.

24. Potero ana a Israyeli anayandikira ana a Benjamini m'mawa mwace.

25. Ndipo Benjamini anawaturukira ku Gibeya m'mawa mwace, naononganso a ana a Israyeli amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga.

26. Pamenepo ana onse a Israyeli ndi anthu onse anakwera nafika ku Beteli, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.

27. Ndipo ana a Israyeli anafunsira kwa Yehova; pakuti likasa la cipangano la Mulungu linakhala komweko masiku aja,

28. namaima ku likasalo Pinehasi mwana wa Eleazare mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditurukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.

29. Ndipo Israyeli anaika olalira Gibeya pozungulira pace.

Oweruza 20