Oweruza 20:13-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pace, okhala m'Gibeya, kuti tiwaphe, ndi kucotsera Israyeli coipaci. Koma Benjamini sanafuna kumvera mau a abale ao, ana a Israyeli.

14. Ndipo ana a Benjamini anasonkhana kucokera ku midzi kumka ku Gibeya, kuti aturuke kulimbana ndi ana a Israyeli.

15. Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m'midzi tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala m'Gibeya, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri.

16. Mwa anthu awa onse munali amuna osankhika mazana asanu ndi awiri amanzere, yense wa iwo amaponya mwala mwa maluli osaphonya.

17. Ndipo anawerenga amuna a Israyeli, osati Benjamini, amuna zikwi mazana anai osolola lupanga, anthu a nkhondo okha okha.

18. Nauka ana a Israyeli, nakwera kumka ku Beteli, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.

19. Nauka ana a Israyeli m'mawa, naumangira Gibeya misasa.

20. Ndipo amuna a Israyeli anaturuka kulimbana ndi Benjamini; ndi amuna a Israyeli anawandandalikira nkhondo ku Gibeya.

21. Pamenepo ana a Benjamini anaturuka m'Gibeya, naononga a Israyeli tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi,

22. Koma anthu, ndiwo amuna a Israyeli, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.

23. Ndipo ana a Israyeli anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.

24. Potero ana a Israyeli anayandikira ana a Benjamini m'mawa mwace.

25. Ndipo Benjamini anawaturukira ku Gibeya m'mawa mwace, naononganso a ana a Israyeli amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga.

26. Pamenepo ana onse a Israyeli ndi anthu onse anakwera nafika ku Beteli, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.

Oweruza 20