8. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zace zana ndi khumi.
9. Ndipo anamuika m'malire a colowa cace m'Timinatiheresi, ku mapiri a Efraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.
10. Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena nchitoyi adaicitira Israyeli,
11. Ndipo ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala;
12. nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawaturutsa m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.
13. Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndi Asitaroti.
14. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.
15. Kuli konse anaturuka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.
16. Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m'dzanja la iwo akuwafunkha.
17. Koma sanamvera angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu yina, naigwadira; anapambuka msanga m'njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa.