Oweruza 2:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kucokera ku Giligala kumka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kucokera ku Aigupto, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola cipangano canga nanu ku nthawi yonse;

2. ndipo inu, musamacita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvera mau anga; mwacicita ici cifukwa ninji?

3. Cifukwa cacenso ndinati, Sindidzawapitikitsa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.

4. Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israyeli, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.

5. Potero analicha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.

6. Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israyeli anamuka, yense ku colowa cace, dziko likhale lao lao.

7. Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa ndi masiku onse a akulu akulu otsala atafa Yoswa, amene adaona nchito yaikuru yonse ya Yehova anaicitira Israyeli.

Oweruza 2