17. Pamene anakweza maso ace anaona munthu wa pa ulendoyo m'khwalala la mudzi; ndi nkhalambayo inati, Umuka kuti? ufumira kuti?
18. Ndipo ananena nayo, Tirikucokera ku BetelehemuYuda, kumka ku mbali za mapiri a Efraimu, ndiko ndifumira ine; koma ndidamuka ku Betelehemu-Yuda; ndipo tsopano ndiri kumuka ku nyumba ya Yehova; koma palibe munthu wondipatsa nyumba.
19. Ngakhale maudzu ndi cakudya ca aburu athu ziriko; ndi mkate ndi vinyo zirikonso kwa ine ndi kwa mdzakazi wako ndi kwa mnyamata wokhala ndi aka polo ako; kosasowa kanthu.
20. Ndipo nkhalambayo inati, Mtendere ukhale ndi iwe, komatu, zosowa zako zonse ndidzakuparsa ndi ine; pokhapo usa gone m'khwalala.
21. Pamenepo anamlonga m'nyumba yace, napatsa aburu cakudya; ndipo iwo anasamba mapazi ao, nadya, namwa.
22. Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mudziwo, ndiwo anthu otama zopanda pace, anazinga nyumba, nagogodagogoda pacitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Turutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe.
23. Ndipo munthu mwini nyumba anawaturukira nanena nao, lai, abale anga, musacite coipa cotere; popeza mwamuna uyu walowa m'nyumba mwanga, musacite copusa ici.
24. Taonani, mwana wanga wamkazi ndiye namwali, ndi mkazi wace wamng'onoyo siwa; ndiwaturutse iwo, muwacepetse iwo, ndi kuwacitira monga muyesa cokoma; koma mwamuna uyu musamcitire copusa ici.
25. Koma amunawo sanafuna kumvera; motero munthuyu anagwira mkazi wace wamng'ono, naturuka naye kwa iwo kunja; namdziwa iwo, nacita naye zoipa usiku wonse mpaka m'mawa; namlola acoke mbandakuca.
26. Nadza mkaziyo kutaca, nagwa pakhomo pa nyumba ya munthu padali mbuye wace, kufikira kutayera.