Oweruza 15:15-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo anapeza cibwano catsopano ca buru, natambasula dzanja lace nacigwira, nakantha naco amuna cikwi cimodzi.

16. Nati Samsoni,Ndi cibwano ca buru, miuru miuru,Amuna cikwi ndawakantha ndi cibwano ca buru.

17. Ndipo kunali, atatha kunena, anataya cibwano m'dzanja lace; nawacha maiowo Ramati-leki ndiko kunena citunda ca cibwano.

18. Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu cipulumutso ici cacikuru ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa?

19. Pamenepo Mulungu anang'amba pokumbika paja pit Leki, naturukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wace, natsitsimuka iye; cifukwa cace anawacha dzina lace, Kasupe wa wopfuula, ndiwo m'Leki mpaka lero lino.

20. Ndipo Samsoni anaweruza Israyeli m'masiku a Afilisti zaka makumi awiri.

Oweruza 15