6. Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwana wa mbuzi, wopandakanthu m'dzanjaliace; koma sanauza atate wace kapena amai wace cimene adacicita.
7. Ndipo anatsika nakamba ndi mkazi, namkonda Samsoni pamaso pace.
8. Atapita masiku ndipo anabweranso kudzamtenga, napambuka iye kukaona mtembo wa mkango; ndipo taona, m'citanda ca mkango munali njuci zoundana, ndi uci.
9. Ndipo anaufula ndi dzanja lace, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wace ndi amai wace, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauza kuti adaufula uciwo m'citanda ca mkango.
10. Ndipo atate wace anatsikira kwa mkazi; ndi Samsoni anakonzerapo madyerero; pakuti amatero anyamata.
11. Ndipo kunali, pamene anamuona, anabwera nao anzace makumi atatu akhale naye.
12. Nanena nao Samsoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kuukumika uwu, ndidzakupatsani malaya a nsaru yabafuta makumi atatu, ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu;
13. koma ngati simukhoza kunditanthauzira uwu mudzandipatsa ndinu Malaya a nsaru yabafuta makumi atatu ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu. Pamenepo ananena naye, Mwambi wako tiumve.