16. Ndipo mkazi wa Samsoni analira pamaso pace, nati, Ungondida, osandikonda; waphera anthu a mtundu wanga mwambi, osanditanthauzira ine. Ndipo ananena naye, Taona, sindinatanthauzira atate wanga kapena amai wanga, kodi ndikutanthauzire iwe?
17. Ndipo analira pamaso pace masiku asanu ndi awiriwo pocitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lacisanu ndi ciwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wace mwambiwo.
18. Ndipo amuna a pamudzi anati kwa Samsoni tsiku lacisanu ndi ciwiri, lisanalowe dzuwa, Cozuna coposa uci nciani; ndi camphamvu coposa mkango nciani? Pamenepo ananena nao,Mukadapanda kulima ndimthandi wanga,Simukadakumika mwambi wanga.