Oweruza 13:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m'munda, mwanuna wace Manowa palibe.

10. Ndipo mkaziyo anafulumira nathamanga, nauza mwamuna wace, nanena naye, Taona, wandionekera munthu anandidzerayo tsiku lija.

11. Nanyamuka Manowa natsata mkazi wace, namdzera mwamuna uja, nanena naye, Kodi ndinu mwamuna ujamunalankhulandimkaziyu? Ndipo anati, Ndine amene.

12. Nati Manowa, Acitike tsopano mau anu; koma makhalidwe ace a mwanayo ndi macitidwe ace adzatani?

13. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Zonse ndinazinena ndi mkazi azisamalire.

14. Ciri conse cicokera kumpesa asadyeko, asamwe vinyo kapena coledzeretsa, kapena kudya ciri conse codetsa; zonse ndinamlamulira azisunge.

15. Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Tiloleni tikucedwetseni kuti tikukonzereni mwana wa mbuzi.

16. Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undicedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwa kuti ndiye mthenga wa Yehova.

17. Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Dzina lanu ndani, kuti, atacitika mau anu, tikucitireni ulemu.

18. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ufunsiranji dzina langa, popeza liri lodabwitsa?

Oweruza 13