Oweruza 12:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo amuna a Efraimu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriraoji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndimotopamtupako.

2. Ndipo Yefita anati kwa iwo, Ine ndi anthu anga tinatsutsana kwakukuru ndi ana a Amoni, koma pamene ndinakuitanani inu simunandipulumutsa m'dzanju lao.

3. Ndipo pakuona ine kuti simunandipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundicitira nkhondo?

4. Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Gileadi nalimbana naye Efraimu; ndipo amuna a Gileadi anakantha Efraimu, cifukwa adati, Inu Agileadi ndinu akuthawa Efraimu, pakati pa Efraimu ndi pakati pa Manase.

Oweruza 12