Oweruza 11:32-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Potero Yefita anapita kwa ana a Amoni kuwathira nkhondo; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja lace;

33. nawakantha kuyambira ku Aroeri mpaka ufika ku Miniti, ndiyo midzi makumi awiri, ndi ku Abelikerami, makanthidwe akuru ndithu. Motero ana a Amoni anagonjetsedwa pamaso pa ana a Israyeli.

34. Pofika Yefita ku Mizipa ku nyumba yace, taonani, mwana wace wamkazi anaturuka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wace mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.

35. Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zobvala zace, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukuru, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.

Oweruza 11