Oweruza 11:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi ciani ndi Inu, ndi kuti Mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa?

13. Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Cifukwa Israyeli analanda dziko langa pakukwera iye kucokera ku Aigupto, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordano; ndipo tsopano uodibwezere maikowa mwamtendere.

14. Ndipo Yefita anatumanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni;

15. nanena naye, Atero Yefita, Israyeli sanalanda dziko la Moabu kapena dziko la ana a Amoni;

16. pakuti pakukwera iwo kucokera ku Aigupto Israyeli anayenda m'cipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi;

17. pamenepo Israyeli anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu sinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Moabu; nayenso osalola; ndipo Israyeli anakhala m'Kadesi.

18. Pamenepo anayenda m'cipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Moabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Moabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Moabu, pakuti Arinoni ndi malire a Moabu.

19. Ndipo Israyeli anatuma mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, mfumu ya ku Hesiboni; nanena naye Israyeli, Tikupemphani tipitire pakati pa dziko lanu, kumka kwathu.

Oweruza 11