10. Ndipo akuru a Gileadi anati kwa Yefita, Yehova ndiye wakumvera pakati pa ife, tikapanda kucita monga momwe wanena.
11. Pamenepo Yefita anamuka ndi akuru a Gileadi, ndipo anthu anamuika mkuru wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ace onse pamaso pa Yehova ku Mizipa.
12. Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi ciani ndi Inu, ndi kuti Mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa?
13. Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Cifukwa Israyeli analanda dziko langa pakukwera iye kucokera ku Aigupto, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordano; ndipo tsopano uodibwezere maikowa mwamtendere.
14. Ndipo Yefita anatumanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni;
15. nanena naye, Atero Yefita, Israyeli sanalanda dziko la Moabu kapena dziko la ana a Amoni;
16. pakuti pakukwera iwo kucokera ku Aigupto Israyeli anayenda m'cipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi;
17. pamenepo Israyeli anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu sinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Moabu; nayenso osalola; ndipo Israyeli anakhala m'Kadesi.
18. Pamenepo anayenda m'cipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Moabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Moabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Moabu, pakuti Arinoni ndi malire a Moabu.
19. Ndipo Israyeli anatuma mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, mfumu ya ku Hesiboni; nanena naye Israyeli, Tikupemphani tipitire pakati pa dziko lanu, kumka kwathu.
20. Koma Sihoni sanakhulupirira Israyeli kuti apitire pakati pa malire ace; koma Sihoni anamemeza anthu ace onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israyeli.