Nyimbo 8:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndaniyu acokera kucipululu,Alikutsamira bwenzi lace?Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe:Pomwepo amako anali mkusauka nawe,Pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.

6. Undilembe pamtima pako, mokhoma cizindikilo, nundikhomenso cizindikilo pamkono pako;Pakuti cikondi cilimba ngati imfa;Njiru imangouma ngati manda:Kung'anima kwace ndi kung'anima kwa moto,Ngati mphezi ya Yehova,

7. Madzi ambiri sangazimitse cikondi,Ngakhale mitsinje yodzala kucikokolola:Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yace ngati sintho la cikondi,Akanyozedwa ndithu.

8. Tiri ndi mlongwathu wamng'ono,Alibe maere;Ticitirenji mlongwathuTsiku lokhoma unkhoswe wace?

9. Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva:Ngati ndiye citseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.

Nyimbo 8