Nyimbo 4:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Taona, wakongola, bwenzi langa, namwaliwe, taona, wakongola;Maso ako akunga a nkhunda patseri pa cophimba cako:Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,Zooneka pa phiri la Gileadi.

2. Mano ako akunga gulu la nkhosa zosengasenga,Zokwera kucokera kosamba;Yonse iri ndi ana awiri,Palibe imodzi yopoloza.

3. Milomo yako ikunga mbota yofiira,M'kamwa mwako ndi kukoma:Palitsipa pako pakunga phande la khangazaPatseri pa cophimba cako.

Nyimbo 4