Nyimbo 3:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndaniyu akwera kuturuka m'cipululu ngati utsi wa tolo,Wonunkhira ndi nipa ndi mtanthanyerere,Ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?

7. Taonani, ndi macila a Solomo;Pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi,A mwa ngwazi za Israyeli.

8. Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo:Yense ali ndi lupanga lace pancafu pace,Cifukwa ca upandu wa usiku.

9. Solomo mfumu anadzipangira macila okhalamo tsongaNdi matabwa a ku Lebano.

10. Anapanga timilongoti tace ndi siliva,Ca pansi pace ndi golidi, mpando wace ndi nsaru yakuda,Pakati pace panayalidwa za cikondi ca ana akazi a ku Yerusalemu.

11. Turukani, ana akazi inu a Ziyoni, mupenye Solomo mfumu,Ndi korona amace anambveka naye tsiku la ukwati wace,Ngakhale tsiku lakukondwera mtima wace.

Nyimbo 3