Nyimbo 3:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda:Ndinamfunafuna, koma osampeza.

2. Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m'mudzi,M'makwalala ndi m'mabwalo ace,Ndimfunefune amene moyo wanga umkonda:Ndimfunafuna, koma osampeza.

3. Alonda akuyendayenda m'mudzi anandipeza:Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?

4. Nditawapitirira pang'ono,Ndinampeza amene moyo wanca umkonda:Ndinamgwiriziza, osamfumbatula,Mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai,Ngakhale m'cipinda ca wondibala.

5. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Pali mphoyo, ndi nswala ya kuthengo,Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi,Mpaka cikafuna mwini.

Nyimbo 3