4. Anandifikitsa ku nyumba ya vinyo,Mbendera yace yondizolimira inali cikondi.
5. Mundilimbikitse ndi mphesa zouma, munditonthoze mtima ndi maula,Pakuti ndadwala ndi cikondi.
6. Dzanja lace lamanzere anditsamiritse kumutu,Dzanja lace lamanja ndi kundifungatira.
7. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Pali mphoyo, ndi nswala za kuthengo,Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi,Mpaka cikafuna mwini.
8. Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza,Alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda.
9. Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala:Taona, aima patseri pa khoma pathu,Apenyera pazenera, Nasuzumira pamade.
10. Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine,Tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye.