Nyimbo 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. NYIMBO yoposa, ndiyo ya Solomo.

2. Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwace;Pakuti cikondi cako ciposa vinyo.

3. Mafuta ako anunkhira bwino;Dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa;Cifukwa cace anamwali akukonda.

4. Undikoke; tikuthamangire;Mfumu yandilowetsa m'zipinda zace:Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe.Tidzachula cikondi cako koposa vinyo:Akukonda molungama.

5. Wakuda ine, koma wokongola,Ana akazinu a ku Yerusalemu,Ngati mahema a Kedara,Ngati nsaru zociriga za Solomo.

6. Musayang'ane pa ine, pakuti ndada,Pakuti dzuwa landidetsa.Ana amuna a amai anandikwiyira,Anandisungitsa minda yamipesa;Koma munda wanga wanga wamipesa sindinausunga.

7. Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda,Umaweta kuti gulu lako?Umaligonetsa kuti pakati pa usana?Pakuti ndikhalirenji ngati wosoceraPambali pa magulu a anzako?

Nyimbo 1