84. Uku ndi kupereka ciperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israyeli, tsiku la kudzoza kwace: mbizi zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolidi khumi ndi ziwiri;
85. mbizi yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.
86. Zipande zagolidi ndizo khumi ndi ziwiri, zodzala ndi cofukiza, cipande conse masekeli khumi, kuyesa sekeli wa malo opatulika; golidi wonse wa zipandezo ndiwo masekeli zana limodzi ndi makumi awiri;