Numeri 7:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Wakubwera naco copereka cace tsiku loyamba ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu, wa pfuko la Yuda:

13. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembeyaufa;

14. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

15. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

16. ronde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

17. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa: asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Nahesoni mwana wa Aminadabu.

18. Tsiku laciwiri Netaneli mwana wa Zuwara, kalonga wa Isakara, anabwera naco cace:

19. anabwera naco copereka cace mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

Numeri 7