Numeri 4:19-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulikitsazo; Aroni ndi ana ace amuna alowe, namuikire munthu yense nchito yace ndi katundu wace.

20. Koma asalowe kukaona zopatulikazo pozikulunga, kuti angafe.

21. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

22. Werenganso ana a Gerisoni, monga mwa nyumba za makolo ao, monga mwa mabanja ao.

23. Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kucita nchitoyi m'cihema cokomanako.

24. Nchito ya mabanja a Agerisoni, pogwira nchito ndi kusenza katundu ndi iyi;

25. azinyamula nsaru zophimba za kacisi, ndi cihema cokomanako, cophimba cace, ndi cophimba ca zikopa za akatumbu ciri pamwamba pace, ndi nsaru yotsekera pa khomo la cihema cokomanako;

Numeri 4