7. Midzi yonse muipereke kwa Alevi ndiyo midzi makumi anai ndi isanu ndi itatu, iyo pamodzi ndi mabusa ao.
8. Ndipo kunena za midziyo muiperekeyo yao yao ya ana a Israyeli, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako midzi yao kwa Alevi monga mwa colowa cao adacilandira.
9. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
10. Nenandi ana a Israyeli, nuti nao, Pakuoloka inu Yordano kulowa m'dziko la Kanani,
11. muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzace wosati dala athawireko.