Numeri 32:39-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Ndipo ana a Makiri mwana wa Manase anamka ku Gileadi, naulanda, napitikitsa Aamori anali m'mwemo.

40. Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Gileadi; ndipo anakhala m'menemo.

41. Ndipo Yairi mwana wa Manase anamka nalanda midzi yao, naicha Havoti Yairi. Ndipo Noba anamka nalanda Kenati, ndi miraga yace, naucha Noba, dzina lace.

Numeri 32