32. Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pa malo opatulika.
33. Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo a Merari; ndiwo mabanja a Merari.
34. Ndipo owerengedwa ao, powerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi kudza mazana awiri.
35. Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja a Merari ndiye Zuriyeli mwana wa Abiyaili; azimanga mahema ao pa mbali ya kacisi ya kumpoto.
36. Ndipo coyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a kacisi, ndi mitanda yace, ndi mizati ndi nsanamira zace, ndi makamwa ace, ndi zipangizo zace zonse, ndi nchito zace zonse;