35. Tsiku lacisanu ndi citatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamacita nchito ya masiku ena;
36. koma mubwere nayo nsembe yopsereza ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri, a caka cimodzi, opanda cirema;
37. nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;
38. ndi tonde mmodzi wa nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.