18. ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;
19. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira.
20. Ndi tsiku lacitatu ng'ombe khumi ndi imodzi, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai a caka cimodzi opanda cirema;
21. ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;