Numeri 27:15-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo Mose ananena ndi Yehova, nati,

16. Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, aike munthu pa khamulo,

17. wakuturuka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwaturutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Ambuye lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.

18. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;

19. numuimike pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; numlangize pamaso pao.

20. Ndipo umuikirepo ulemerero wako, kuti khamu lonse la ana a Israyeli ammvere.

Numeri 27