Numeri 26:40-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Ndipo ana amuna a Bela ndiwo Aridi ndi Namani; Aridi, ndiye kholo la banja la Aaridi; Namani, ndiye kholo la banja la Anamani.

41. Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi.

42. Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ace ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao.

Numeri 26