28. Ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efraimu.
29. Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Gileadi; ndiye kholo la banja la Agileadi,
30. Ana a Gileadi ndiwo: Yezeri, ndiye kholo la banja la Ayezeri; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki;
31. ndi Asiriyeli, ndiye kholo la banja la Aasiriyeli; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu;
32. ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Heferi, ndiye kholo la banja la Aheferi.