17. Ndimuona, koma tsopano ai; Ndimpenya, koma si pafupi ai;Idzaturuka nyenyezi m'Yakobo,Ndi ndodo yacifumu idzauka m'Israyeli,Nidzakantha malire a Moabu,Nidzapasula ana onse a Seti,
18. Ndi Edomu adzakhala ace ace,Seiri lomwe lidzakhala lace lace, ndiwo adani ace;
19. Koma Israyeli adzacita zamphamvu.Ndipo wina woturuka m'Yakobo adzacita ufumu;Nadzapasula otsalira m'mudzi.
20. Ndipo anayang'ana ku Amaleki, nanena fanizo lace, nati,Amaleki ndiye woyamba wa amitundu;Koma citsiriziro cace, adzaonongeka ku nthawi zonse.
21. Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lace, nati,Kwanu nkokhazikika,Wamanga cisa cako m'thanthwe.
22. Koma Kaini adzaonongeka,Kufikira Asuri adzakumanga nsinga.