11. Pamenepo Balaki anati kwa Balamu, Wandicitiranji? Ndinakutenga utemberere adani anga, ndipo taona, wawadalitsa ndithu.
12. Ndipo anayankha nati, Cimene aciika m'kamwa mwanga Yehova, sindiyenera kodi kunena ici?
13. Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.
14. Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa pa guwa la nsembe liri lonse.
15. Ndipo anati kwa Balaki, Imani pano pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine ndikakomane ndi iye uko.
16. Ndipo Yehova anakomana naye Balamu, naika mau m'kamwa mwace, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene cakuti cakuti.
17. Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yace yopsereza, ndi akalonga a Moabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?
18. Ndipo ananena fanizo lace, nati,Ukani, Balaki, imvani;Ndimvereni, mwana wa Zipori;
19. Mulungu sindiye munthu, kuti aname;Kapena mwana wa munthu, kuti aleke;Kodi anena, osacita?