Numeri 21:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kuticotsa ku Aigupto kuti tifere m'cipululu? pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wacabe uwu.

6. Pamenepo Yehova anatumiza njoka zamoto pakati pa anthu, ndipo zinaluma anthu; nafapo anthu ambiri a Israyeli.

7. Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tacimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti aticotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.

8. Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Upange njoka yamoto; nulike pa mtengowace; ndipo kudzali, kuti onse olumwa, akuipenya njokayo, adzakhala ndi moyo.

9. Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu ali yense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.

10. Pamenepo ana a Israyeli anayenda ulendo, namanga mahema m'Oboti.

11. Ndipo anacoka ku Oboti, namanga mahema ku Iyebarimu, m'cipululu cakuno ca Moabu, koturukira dzuwa.

12. Pocokapo anayenda ulendo, namanga mahema m'cigwa ca Zaredi.

13. Atacokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya tina la Arinoni, wokhala m'cipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Moabu, pakati pa Moabu ndi Aamori.

Numeri 21