4. Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'cipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?
5. Ndipo munatikwezeranji kutiturutsa m'Aigupto, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.
6. Ndipo Mose ndi Aroni anacoka pamaso pa msonkhano kumka ku khomo la cihema cokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.
7. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
8. Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwaturutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.