9. Ndipo Mose anaturutsa ndodo zonse kuzicotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israyeli; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yace.
10. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kulika cakuno ca mboni, isungike ikhale cizindikilo ca pa ana opikisana; kuti unelitsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.
11. Ndipo Mose anacita monga Yehova adamuuza, momwemo anacita.
12. Pamenepo ana a Israyeli ananena ndi Mose, nati, Taonani, tikufa, tionongeka, tionongeka tonse.
13. Yense wakuyandikiza kacisi wa Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa?