Numeri 16:22-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?

23. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

24. Nena ndi khamulo, ndi kuti, Kwerani kucoka pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu.

Numeri 16