35. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Amuphe munthuyu ndithu; khamu lonse limponye miyala kunja kwa cigono.
36. Pamenepo khamu lonse linamturutsa kunja kwa cigono, ndi kumponya miyala, ndipo anafa; monga Yehova adauza Mose.
37. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
38. Nena ndi ana a Israyeli, nuwauze kuti adziombere mphonje m'mphepete mwa zobvala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m'mphepetemo thonje lamadzi.