10. Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu cikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
11. Ndipo kunacitika, caka caciwiri, mwezi waciwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kucokera kwa kacisi wa mboni.
12. Ndipo ana a Israyeli anayenda monga mwa maulendo ao, kucokera m'cipululu ca Sinai; ndi mtambo unakhala m'cipululu ca Parana.
13. Potero anayamba ulendo wao monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.
14. Ndipo anayamba kuyenda a mbendera ya cigono ca ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lace ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu.
15. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Isakara panali Netaneli mwana wa Zuwara.