72. Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolidi zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri, ndi maraya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri.
73. Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oyimbira, ndi anthu ena, ndi Anetini, ndi Aisrayeli onse.Utakhala tsono mwezi wacisanu ndi ciwiri ana a Israyeli anakhala m'midzi mwao.