31. Amuna a ku Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.
32. Amuna a ku Betele ndi Ai, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.
33. Amuna a ku Nebo winayo, makumi asanu kudza awiri.
34. Ana a Elamu winayo, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai.
35. Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri.
36. Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu.
37. Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza mmodzi.