1. Pamenepo panamveka kulira kwakukuru kwa anthu ndi akazi ao kudandaula pa abale ao Ayuda.
2. Popeza panali ena akuti, Ife, ana athu amuna ndi akazi, ndife ambiri; talandira tirigu, kuti tidye tikhale ndi moyo.
3. Panali enanso akuti, Tirikupereka cikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu cifukwa ca njalayi.