Nehemiya 3:31-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golidi kufikira ku nyumba ya Anetini, ndi ya ocita malonda, pandunji pa cipata ca Hamifikadi, ndi ku cipinda cosanja ca kungondya.

32. Ndi pakati pa cipinda cosanja ca kungondya ndi cipata cankhosa anakonza osula golidi ndi ocita malonda.

Nehemiya 3