Nehemiya 3:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Eliasibu mkuru wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ace ansembe, namanga cipata cankhosa; anacipatula, naika zitseko zace, inde anacipatula mpaka nsanja ya Mea, mpaka nsanja ya Hananeeli.

2. Ndi pambali pace anamanga amuna a ku Yeriko. Ndi pambali pao anamanga Zakuri mwana wa Imri.

Nehemiya 3