33. kuliperekera mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israyeli zoipa, ndi nchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.
34. Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a copereka ca nkhuni, kubwera nazo ku nyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika caka ndi caka, kuzisonkha pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'cilamulo;
35. ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uli wonse caka ndi caka, ku nyumba ya Yehova;