11. Iri kuti ngaka ya mikango, ndi podyera misona ya mikango; kumene mkango, waumuna ndi waukazi, ukayenda ndi mwana wa mkango, kopanda wakuiposa?
12. Mkangowo unamwetula zofikira ana ace, nusamira yaikazi yace, nudzaza mapanga ace ndi nyama, ngaka zace ndi zojiwa.
13. Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magareta ace m'utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzacotsa zofunkha zako pa dziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.